Mphunzitsi wa timu ya CRECK Sporting Club, Enerst Mtawali wati kukonderedwa kwa matimu ena mdziko muno, ndi china mwa zifukwa zomwe zikupangitsa kuti timu ya dziko lino isamachite bwino.
Mtawali amayankhula izi pa bwalo la zamasewero la Mpira mu mzinda wa Blantyre pomwe timu yake yagonja kwa Mighty Wanderers ndi chigoli chimodzi kwa duu chomwe anagoletsa ndi Peter Ng’ambi, mu FDH Premiership.
Iye wati pali zambiri zomwe woyimbira, Cedric Mwachumu anachita, pofuna kuyipatsa mpata Wanderers kuti ipate ma point onse mmasewerowa.
“Tidziwe kuti Flames sikuchita bwino, pamafunika timu imene yachita bwino ipambane, pasamakhale anthu ena othandizira timu kuti ipambane. Ife ndi timu yaying’ono, timakhulupira kupambana bwinobwino, ndimmene mpira ukuyenera kumayendera” anatero Mtawali.
Katswiri wakale wa Flames yu anati woyimbira samayimba nthawi zambiri ngati Mighty Wanderers yalakwitsa.
Iye wati timu yake sikufuna kukonderedwa kuti ikhalebe mu ligi yayikulu ndipo anati izi zokufunikaso zizichitika ku Mighty Wanderers ngati timu yayikulu kuti idzipeza chipambano moyenera.
