… aMalawi ali nganganga pambuyo pa Suleman
Yatangwanika zedi nduna yofalitsa nkhani a Shadric Namalomba kuikira kumbuyo akuluakulu aboma pa nkhani yoti nduna ndi akuluakulu ena akususa kwambiri pa ndalama za misonkho ya a Malawi. Koma aMalawi sakugwirizana ndi ganizoli.
Posachedwapa, sipikala wa nyumba ya malamulo Sameer Suleman, adayankhula pa mwambo wina kudzudzula mchitidwe waumbava pakati pa mamulumuzana ena m’bomamu.
Mawu a Suleman adatokosola mavu nkhomola. Namalomba adauza Suleman kuti pasanathe masiku asanu ndi awiri apereke umboni wa zomwe wayankhulazo ponena kuti palibe akuba ndalama m’boma.
Khale khale, naye mtsogoleri wa chipani cha UTM Dalitso Kabambe, adadzudzula mchitidwe waumbava m’bomamu.
Popitilira kuikira boma kumbuyo, Namalomba watulutsa kalata momwe wati boma lotsogozedwa ndi a Peter Mutharika silisekerera akuluakulu aboma onse omwe akuchita katangale.
“Purezidenti wa dziko la Malawi, Peter Mutharika, adanena momveka bwino kuti palibe nduna ya boma, akuluakulu a boma, wogwira ntchito m’boma kapena munthu wina aliyense amene adzatetezedwe kuti asafufuzidwe kapena kuimbidwa mlandu motsatira malamulo. Palibe munthu amene ali pamwamba pa malamulo,” watero Namalomba.
Apa, Namalomba wapempha anthu onse omwe Ali ndi umboni woti m’boma muli katangale kuti akatsine khutu nthambi yofufuza za katangale ya Anti Corruption Bureau (ACB).
“Boma likupempha anthu amene akunena za ziphuphuzi kuti asiye kungolankhula pagulu, koma apereke umboni wawo ku Bungwe la ACB kapena ku polisi,” wateroso Namalomba.
Izi zakwiitsa a Malawi ena omwe akuti sizofunikiraso kupereka umboni, ponena kuti aliyese akuona zomwe zikuchitika.
“Umboni wawukulu ndi jaji amene anapeleka chiletso kuti parliament isakhazikitse commission of inquiry ku nthambi za boma. Anawopanji?” adatero Ahmad Ismael Makonope poikira ndemanga pa tsamba lathu la fesibuku.
Naye Dickson Rashid sanafune kupsatira mawu. “Ndiye mumamangidwa? Zaziiii nkhan ndikusintha cystem, ku court kuliso corruption, deal ndikusintha boma ndi kukhazikitsidwa malamulo okhwima, wakuba misonkho ya Malawi aphedwa. Osati zokutengelan kuma bwalo omwe akupangidwa control ndi andale. Anamalombatu mukuwonjezatu mukudzimva mphavu, pomwe dela lomwe mu kuchokela palibe chomwe mu kuchita. Opepela ndi anthu akumangochi pokupatsan MP, kaya kusaphudzila anthu a kwathu.”
Mawu a Namalomba akutsutsana ndizomwe zachitika posachedwapa pomwe boma lakanitsitsa mwantu wagalu ganizo la a Suleman lokhazikitsa ma komiti a apadera oti afufuze kagwiridwe ntchito ka nthambi zina za boma.
Akuluakulu ena a boma kuphatikizapo a Namalomba, akhala akudzudzuka a Suleman kuti ganizo lawoli ndi chisonyezo choti nyumba ya malamulo ikulowerera ntchito zomwe siidapangidwire.
Koma kafukufuku amene tinapanga pa tsamba lathu la fesibuku sabata ino, wasonyeza kuti a Malawi ambiri ali pa mbuyo pa a Suleman.
Mwa anthu pafupifupi 5000 omwe anatenga gawo pa kafukufukuyu, oposa 3,500 adati Ali nganganga pambuyo pa sipikala wa nyumba ya malamuloyu.
