Agwidwa njakata aphunzitsi ndi ophunzira pa sukulu ya Nthema Primary, kudera la mfumu yaikulu Wimbe ku Kasungu komwe mjigo sukumva kukonzedwa.
Pomwe azanyengo akulimbikitsa anthu kumwa madzi pafupifu pafupi kamba ka kutentha konyanyira, kupeza madziwa pakati pa ophunzira pa sukuluyi ndi ntchito ya padera kamba ka mjigowu omwe tsopano ndi bwenzi la mphasa.
Malingana ndi mphunzitsi wina pasukuluyi, yemwe wapempha kusatchulidwa dzina, kwa nthawi yaitali mjigowu wakhala ukuwonongeka pafupifu pafupi.
Iye wati ndalama zomwe aphunzitsi akhala akusonkherana mwezi uliwonse zokozetsera mjigowu, zakhala zikungolowa m’madzi poti akawukoza, mjigowu umawonongekaso pakangodutsa masiku ochepa.
Iye wati kwa nthawi yaitali, vutoli lakhala likusokoneza ntchito zaukhondo pa sukuluyi, kuika miyoyo ya ophunzira pa chiopsezo chotenga matenda okhudzana ndi ukhondo.
Mphunzitsiyu wati mwezi uno wa October zinthu siziri bwino pa sukuluyi pomwe mjigowu wakhala milungu itatu tsopano uli chiwonongekere.
Iye wati pano ophunzira akuzuzika ndi nyengo yotentha ndipo wati pano ophunzira akukakamizika kumakatunga madzi pa mjigo wa m’mudzi.
“Panopa tingoti tilibe mjigo wathu pasukulu pano. Ana asukulu amakakamizika kupita kukatunga madzi ku mjigo wa kumudzi, zomwe zikusokoneza maphunziro awo komanso zimawatengera nthawi yomwe akanakhala akuphunzira,” watero mphunzitsiyu.
Mphunzitsiyu wapempha akuluakulu a za maphunziro ndi ena akafuna kwabwino kuti athandize kuthetsa vutoli pa sukuluyi.
