Nduna yofalitsa nkhani yemwenso ndi m’neneri wa boma a Shadric Namalomba apepesa mtundu wa aMalawi chifukwa cha kuzimazima kwa magetsi komwe kukuchitika mdziko lino.
A Namalomba ati boma likuvomereza kuti likuwagoneka anthu mu mdima.
Polankhula ndi wayilesi ya kanema ya Zodiak loweluka a Namalomba ati kuzimazima kwa magetsi ndi vuto lalikulu lomwe akuyesesa kuthana nalo.
“Mwina timachitika tsoka, poti tikamabwera pamalo timapeza anzathu atawononga”. anatero a Namalomba.
Mkulankhula kwawo iwo ati popanga magetsi pamafunika zipangizo zina za mlowammalo za zomwe zikugwira kale ntchito zikawonongeka zina zikhonza kulowa m’malo mwake koma ati izi sizinali choncho ayi.
A Namalomba ati ma kampani opanga magetsi akhala akukanika kugula zipangizo za mlowammalo kuti zizikhaliratu chire, ndipo mapeto ake akhala akungogwiritsa ntchito zomwe zilipozo mpaka zantha ndi mchaka vuto la kuzima kwa magetsi ladza.
Iwo ati izi zachitika kwambiri chifukwa cha kusowa kwa ndalama zakunja.
Ndunayi yavomereza kuti anthu akulephera kupanga zinthu mwa nthawi zonse chifukwa cha magetsi koma ati boma likuyesetsa kuthana nalo vutoli ndipo posachedwa anthu awona magetsi.
Iwo ati mgwirizano wa boma ndi dziko la Mozambique okhudza kugawana magetsi, magetsi a Malasha, a Dzuwa ndi zina zithandizira kuti magetsi abwerere mchimake.
