Patangodutsa masiku ochepa Malawi24 italemba nkhani ya Joseph Nenani Major, wophunzira wa ku University ya Malawi UNIMA yemwe amafuna kudzipha kaamba ka mavuto ndi ngongole, Mayi wa fuko, Gertrude Mutharika wadalitsa wophunzirayu.
Mkazi wa mtsogoleri wa dzikoyu wati anakhudzika kwambiri atamva moyo omwe ophunzirayu amakhala kuyambira pomwe anayamba maphunziro ake mchaka choyamba.
Kutsatira izi, kudzera ku Beautify Malawi Trust BEAM mayi Mutharika Lachitatu apereka katundu osiyanasiyana wa ndalama zoposa 5 million kwacha kwa wophunzirayu m’boma la Zomba.
Polankhula pa mwambo wopereka mphatsozi, calamanco wa bungwe la BEAM Trust a Dingiswayo Jere, anati Mayi wafukoyu amayika maphunziro pamtima pawo.
“Ndi khumbokhumbo la Mayi wadziko lino kuthandiza pa maphunziro ndipo amayesetsa kuti tigawane pang’onopangono kuti wina wapezako kangachepe athandize wina,” anatero a Jere.

Iwo anati Joseph amayenera kupeza chimwemwe pa maphunziro ake, ndipo alimbikitsa kugawana ponena kuti ndi maphunziro okha amene amatha kutsekula mwayi kwa munthu pa dziko.
M’mawu ake atalandira thandizoli Nenani Major wati ndi wokondwa chifukwa BEAM yamupulumutsa mu nyengo zomwe wakhala akudutsamo chiyambiren maphunziro ake.
Iye wati thandizo la BEAM limupangitsa kuti tsopano alunjike pa maphunziro ake okha ponena kuti nthawi zambiri amasakaniza sukulu ndi maganyu kuti apeze zofunika.
Major ndi wophunzira yemwe masabata angapo apitawo analemba kalata yofuna kudzipha chifukwa cha ngongole ya ndalama zokwana K594 sauzande komanso kuchuluka kwa udindo mwa zina zomwe ati zakhala zikumusautsa kwambiri ndipo anasiya kuwona tsogolo.
Major yemwe amayenera akhale atamaliza maphunziro ake mchaka cha 2021/2022, pakadali pano akulimbana nawobe maphunziro a uphunzitsi wa Social Studies ndipo ali mchaka chachitatu.
Wophunzirayu yemwe amachokera m’mudzi mwa a Meja m’boma la Mulanje wati anthu akufuna kwabwino adamuthandiza kulipira ngongole zake zonse.
Wina mwa katundu yemwe BEAM yamupatsa ndi makina a computer ya mmanja, ufa, sugar, Mchere,soap, Mafuta ophikira, Mkaka, zokumwa, chofunda mwa zina.
